50 Iweyo uike Aleviwo kukhala oyang’anira chihema cha Umboni+ ndi ziwiya zake zonse, ndi chilichonse cha mmenemo.+ Iwowo ndi amene azinyamula chihema chopatulikacho ndi ziwiya zake zonse.+ Ndi amenenso azitumikira+ pachihemapo, ndipo azimanga misasa yawo mochizungulira.+