17 Mzindawu wapatulidwa kuti uwonongedwe,+ pakuti mzindawu limodzi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova. Rahabi+ yekha, hule uja, musamuphe. Mum’siye ndi moyo, iye pamodzi ndi onse amene ali naye m’nyumba mwake, chifukwa iye anabisa azondi amene tinawatuma.+