15 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandiperekeze kumene kuli gulu la achifwambali?” Poyankha, iye anati: “Ndilumbirire+ pamaso pa Mulungu kuti sundipha, komanso kuti sundipereka m’manja mwa mbuyanga.+ Ukatero ndikuperekeza kumene kuli gulu la achifwambali.”