Yoswa 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+ 1 Samueli 20:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndipo ine ndikadzakhalabe ndi moyo,+ kodi sudzandisonyeza kukoma mtima kosatha kwa Yehova kuti ndisafe?+ Kodi sudzatero? 1 Samueli 30:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandiperekeze kumene kuli gulu la achifwambali?” Poyankha, iye anati: “Ndilumbirire+ pamaso pa Mulungu kuti sundipha, komanso kuti sundipereka m’manja mwa mbuyanga.+ Ukatero ndikuperekeza kumene kuli gulu la achifwambali.”
14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+
14 Ndipo ine ndikadzakhalabe ndi moyo,+ kodi sudzandisonyeza kukoma mtima kosatha kwa Yehova kuti ndisafe?+ Kodi sudzatero?
15 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandiperekeze kumene kuli gulu la achifwambali?” Poyankha, iye anati: “Ndilumbirire+ pamaso pa Mulungu kuti sundipha, komanso kuti sundipereka m’manja mwa mbuyanga.+ Ukatero ndikuperekeza kumene kuli gulu la achifwambali.”