18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+
3 “‘Chigawo chanu chakum’mwera chiyenera kuyambira kuchipululu cha Zini, kumalire a Edomu.+ Malire anu a kum’mwera ayenera kuchokera kumathero a Nyanja Yamchere,+ kum’mawa.
7 Tembenukani ndi kulowera kudera lamapiri la Aamori+ ndi anthu oyandikana nawo onse okhala ku Araba,+ kudera lamapiri,+ ku Sefela, ku Negebu,+ m’mbali mwa nyanja,+ m’dziko la Akanani+ ndi ku Lebanoni+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+