10 Koma mwamunayo sanavomere kuti agone, ndipo ananyamuka ndi kuyamba ulendo wake. Iye anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Yebusi,+ amene ndi Yerusalemu.+ Pa ulendowu, anali ndi abulu awiri amphongo aja, okhala ndi zishalo, ndipo analinso ndi mdzakazi wake ndi mtumiki wake.