Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+

  • Numeri 33:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+

  • Oweruza 1:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+

  • Oweruza 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Choncho, Yehova analola mitundu imeneyi kukhalabe, osaipitikitsa mwamsanga,+ ndipo sanaipereke m’manja mwa Yoswa.

  • Oweruza 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mulungu anapitirizabe kugwiritsa ntchito mitunduyo poyesa+ Aisiraeli, kuti aone ngati Aisiraeliwo adzamvera malamulo a Yehova amene anaperekedwa kwa makolo awo kudzera mwa Mose.+

  • Oweruza 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pamene ankayandikira Yebusi, dzuwa linali litapendeka ndithu,+ ndipo mtumiki uja anauza mbuye wake kuti: “Tiyeni tipatukire mumzinda uwu wa Ayebusi+ kuti tigone mmenemu.”

  • 2 Samueli 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Patapita nthawi, mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene anali kukhala kumeneko. Ayebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno, pakuti upitikitsidwa ndi anthu akhungu ndi olumala.”+ Mumtima mwawo iwo anali kunena kuti: “Davide sangalowe mumzinda uno.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena