11Ndiyeno Yabini mfumu ya ku Hazori+ atangomva nkhaniyi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni, ndi mfumu ya ku Simironi, ndiponso mfumu ya ku Akasafu.+
10 Kuwonjezera apo, Yoswa anabwerera ndi kukalanda+ mzinda wa Hazori+ n’kupha mfumu yake ndi lupanga.+ Anachita zimenezi chifukwa mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa.
2 Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+
9 Atatero iwo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anawagulitsa+ kwa Sisera+ mkulu wa gulu lankhondo la Hazori, komanso kwa Afilisiti+ ndi kwa mfumu ya Mowabu,+ ndipo onsewa anapitiriza kumenyana nawo.