Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 6:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mfuu yankhondo mwamphamvu,+ ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.”

  • Oweruza 6:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Zitatero, Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova,+ moti anayamba kuliza lipenga+ la nyanga ya nkhosa ndipo Aabi-ezeri+ anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira.

  • 1 Samueli 13:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kenako Yonatani anakantha mudzi wa asilikali+ a Afilisiti+ umene unali ku Geba,+ ndipo Afilisiti anamva zimenezi. Zitatero Sauli analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ m’dziko lonse n’kunena kuti: “Imvani Aheberi inu!”

  • 2 Samueli 2:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa,+ ndipo anthu onse anaima, moti sanapitirizenso kuthamangitsa Isiraeli. Iwo sanayambirenso kumenyana.

  • Yoweli 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Lizani lipenga m’Ziyoni+ amuna inu ndipo fuulani mfuu yankhondo+ m’phiri langa loyera.+ Anthu onse okhala m’dzikoli anjenjemere,+ pakuti tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi!

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena