Oweruza 7:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ochuluka kwambiri kuti ndipereke Amidiyani m’manja mwawo,+ chifukwa mwina Isiraeli angadzitukumule+ pamaso panga ndi kunena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+ 1 Samueli 14:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+ Yesaya 41:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 “Usachite mantha, nyongolotsi iwe+ Yakobo, inuyo amuna a Isiraeli.+ Ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli. Aheberi 11:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Anagonjetsa mphamvu ya moto,+ anathawa lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ analimba mtima pa nkhondo,+ ndiponso anagonjetsa magulu ankhondo a mayiko ena.+
2 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ochuluka kwambiri kuti ndipereke Amidiyani m’manja mwawo,+ chifukwa mwina Isiraeli angadzitukumule+ pamaso panga ndi kunena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+
6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+
14 “Usachite mantha, nyongolotsi iwe+ Yakobo, inuyo amuna a Isiraeli.+ Ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli.
34 Anagonjetsa mphamvu ya moto,+ anathawa lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ analimba mtima pa nkhondo,+ ndiponso anagonjetsa magulu ankhondo a mayiko ena.+