Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 17:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ili ndi pangano limene anthu inu muyenera kulisunga, la pakati pa ine ndi inu, ngakhalenso mbewu yobwera pambuyo pa inu.+ Mwamuna aliyense pakati pa inu azidulidwa.+

  • Oweruza 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma bambo ndi mayi akewo anam’funsa kuti: “Kodi wasowa mkazi pakati pa ana aakazi a abale ako ndi anthu onse a mtundu wathu,+ kuti upite kukatenga mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?”+ Koma Samisoni anauza atate akewo kuti: “Ingonditengerani mkazi ameneyu, chifukwa ndi amene ali woyenera kwa ine?”

  • Oweruza 15:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anayamba kufuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwapereka chipulumutso chachikulu chimenechi m’manja mwa mtumiki wanu.+ Tsopano kodi ndife ndi ludzu, ndigwere m’manja mwa anthu osadulidwa?”+

  • 1 Samueli 17:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Mtumiki wanu anapha zonse ziwiri, mkangowo ndi chimbalangondocho. Mfilisiti wosadulidwayu+ akhalanso ngati chimodzi mwa zilombo zimenezi, chifukwa watonza+ asilikali+ a Mulungu wamoyo.”+

  • 2 Samueli 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Anthu inu musanene zimenezi mumzinda wa Gati.+

      Musalengeze zimenezi m’misewu ya Asikeloni,+

      Kuopera kuti ana aakazi a Afilisiti angasangalale,+

      Kuopera kuti ana aakazi a anthu osadulidwa angakondwere.

  • 1 Mbiri 10:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida+ kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundizunza.”+ Koma womunyamulira zida uja sanafune+ kuchita zimenezo, chifukwa anali kuchita mantha kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake n’kuligwera.+

  • Yeremiya 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena