Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 7:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Usabweretse m’nyumba mwako zinthu zonyansa kuti iwenso ungawonongedwe mofanana ndi zinthuzo. Uzinyansidwa nazo kwambiri ndi kuipidwa nazo+ chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.+

  • 2 Mbiri 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 ndipo anthu anga+ otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa+ n’kupemphera,+ n’kufunafuna nkhope yanga,+ n’kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba+ n’kuwakhululukira tchimo lawo+ ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+

  • 2 Mbiri 15:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Asa atangomva mawu amenewa ndi ulosi wa mneneri Odedi,+ analimba mtima n’kuyamba kuchotsa zinthu zonyansa+ m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi m’mizinda imene analanda m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Anayambanso kukonza guwa lansembe la Yehova limene linali patsogolo pa khonde la nyumba ya Yehova.+

  • 2 Mbiri 33:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anachotsa milungu yachilendo,+ fano+ limene linali m’nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse ansembe+ amene anamanga m’phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu. Kenako, zinthu zimenezi anakazitaya kunja kwa mzinda.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena