Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 14:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma mkaziyo anapitiriza kulira pamaso pa Samisoni kwa masiku 7 a phwandolo. Pamapeto pake, pa tsiku la 7, Samisoni anauza mkaziyo tanthauzo lake chifukwa anamuumiriza.+ Kenako mkaziyo anaulula tanthauzo la mwambiwo kwa anthu a mtundu wake.+

  • Oweruza 16:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse za pansi pa mtima wake,+ kuti: “M’mutu mwanga simunadutsepo lezala,+ chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga.+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kundichokera, ndipo ndingafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.”+

  • Miyambo 25:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kambirana mlandu wako ndi mnzako,+ ndipo usaulule chinsinsi cha munthu wina,+

  • Yeremiya 9:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Aliyense wa inu asamale ndi mnzake,+ ndipo musakhulupirire m’bale aliyense.+ Pakuti munthu aliyense amalanda malo a m’bale wake,+ ndipo munthu aliyense amakhala akuyendayenda kunenera mnzake miseche.+

  • Mika 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Musamakhulupirire anzanu. Musamadalire mnzanu wapamtima.+ Samala zonena zako polankhula ndi amene umagona naye pafupi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena