1 Samueli 20:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+ 1 Samueli 25:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika mofulumira pabulu wake. Iye anagwada pamaso pa Davide ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ Aroma 12:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pokonda abale,+ khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu,+ khalani patsogolo. Aroma 13:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, m’patseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.+
41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+
23 Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika mofulumira pabulu wake. Iye anagwada pamaso pa Davide ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+
10 Pokonda abale,+ khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu,+ khalani patsogolo.
7 Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, m’patseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.+