3 Ndiyeno anthuwo atabwerera kumsasa, akulu a Isiraeli anayamba kunena kuti: “N’chifukwa chiyani lero Yehova watigonjetsa pamaso pa Afilisiti?+ Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova+ ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.”