27 Pamenepo mfumu inapitiriza kuuza Zadoki wansembe kuti: “Iwe ndi wamasomphenya,*+ si choncho kodi? Bwerera kumzinda mu mtendere. Bwerera pamodzi ndi Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. Mubwerere ndi ana anu awiri amene muli nawowa.
15 Pambuyo pake Husai anauza Zadoki+ ndi Abiyatara ansembe, kuti: “Ahitofeli wapereka malangizo kwa Abisalomu ndi akulu a Isiraeli ndipo wanena zakutizakuti, koma malangizo amene ine ndapereka, ndanena zakutizakuti.