2 Samueli 15:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Kenako uthenga unafika kwa Davide wonena kuti: “Ahitofeli nayenso ali pakati pa anthu amene akukonza chiwembu+ pamodzi ndi Abisalomu.”+ Pamenepo Davide anati:+ “Inu Yehova!+ Chonde, sandutsani malangizo a Ahitofeli kuti akhale opusa.”+ 2 Samueli 16:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe. 2 Samueli 17:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Koma Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanawagwiritse ntchito,+ anakwera bulu wake ndi kunyamuka kupita kunyumba yake kumzinda wakwawo.+ Kenako anakonzekeretsa banja lake+ ndipo anadzimangirira+ moti anafa.+ Chotero anaikidwa m’manda+ a makolo ake. 1 Mbiri 27:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Ahitofeli+ anali phungu+ wa mfumu ndipo Husai+ Mwareki+ anali mnzake wa mfumu.+
31 Kenako uthenga unafika kwa Davide wonena kuti: “Ahitofeli nayenso ali pakati pa anthu amene akukonza chiwembu+ pamodzi ndi Abisalomu.”+ Pamenepo Davide anati:+ “Inu Yehova!+ Chonde, sandutsani malangizo a Ahitofeli kuti akhale opusa.”+
23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe.
23 Koma Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanawagwiritse ntchito,+ anakwera bulu wake ndi kunyamuka kupita kunyumba yake kumzinda wakwawo.+ Kenako anakonzekeretsa banja lake+ ndipo anadzimangirira+ moti anafa.+ Chotero anaikidwa m’manda+ a makolo ake.