Genesis 4:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pamenepo Mulungu anati: “N’chiyani chimene wachitachi? Tamvera tsono. Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.+ Genesis 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake. Ekisodo 21:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa ndithu.+ Numeri 35:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+ Numeri 35:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ Deuteronomo 21:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndipo inuyo mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu,+ chifukwa mudzakhala mutachita choyenera pamaso pa Yehova.+
10 Pamenepo Mulungu anati: “N’chiyani chimene wachitachi? Tamvera tsono. Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.+
6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake.
21 kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+
33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+
9 Ndipo inuyo mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu,+ chifukwa mudzakhala mutachita choyenera pamaso pa Yehova.+