6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+