2 Ndiyeno pa tsiku lachitatu anaona munthu wina+ akubwera kuchokera kumsasa, kwa Sauli. Iye anali atang’amba zovala zake+ komanso atadzithira dothi kumutu.+ Atafika kwa Davide, nthawi yomweyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ kenako anagona pansi.