Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu woona,+ ndipo palibenso wina.+

  • 2 Mafumu 17:41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Mitundu imeneyi inali kuopa Yehova,+ koma inali kutumikira zifaniziro zawo zogoba. Mpaka lero, ana awo ndi zidzukulu zawo akuchitabe mmene makolo awo ankachitira.

  • Yesaya 42:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli,+ ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense+ kapena kupereka ulemerero wanga+ kwa zifaniziro zogoba.+

  • Yeremiya 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+

  • Hoseya 10:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Mtima wawo wakhala wachinyengo.+ Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu.

      “Pali wina amene adzathyola maguwa awo ansembe ndipo adzasakaza zipilala zawo zopatulika.+

  • Mateyu 12:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine, ndipo amene sagwira limodzi ndi ine ntchito yosonkhanitsa anthu kwa ine amawabalalitsa.+

  • 1 Akorinto 10:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova*+ komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya “patebulo la Yehova”+ komanso patebulo la ziwanda.

  • 2 Akorinto 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena