30 Chotero Yehova anauza Yehu kuti: “Pa chifukwa chakuti wachita bwino, mwa kuchita zoyenera pamaso panga,+ ndiponso wachitira nyumba ya Ahabu+ mogwirizana ndi zonse za mumtima mwanga, ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.”+