12 Kenako Hiramu anapitiriza kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi,+ chifukwa wapereka kwa Davide mfumu mwana wanzeru, wochenjera, ndi wozindikira,+ yemwe amangire Yehova nyumba ndi kudzimangira nyumba ya ufumu wake.+