20 Koma panalibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa zipilala ziwiri zija,+ chosungiramo madzi chimodzi chija,+ ng’ombe zamkuwa 12+ zija ndi zotengera zokhala ndi mawilo zimene Mfumu Solomo inapangira nyumba ya Yehova.+ Palibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa ziwiya zonsezi.+