9 Pomaliza Adoniya anapereka nsembe+ za nkhosa, ng’ombe, ndi ana a ng’ombe onenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti umene uli pafupi ndi Eni-rogeli.+ Kumeneko anaitanirako abale ake onse, omwe anali ana a mfumu,+ ndi amuna onse a mu Yuda, omwe anali atumiki a mfumu.