10Ndiyeno Samueli anatenga+ botolo ladothi la mafuta ndi kutsanulira mafutawo pamutu wa Sauli, n’kumupsompsona+ ndi kunena kuti: “Yehova wakudzoza iwe kukhala mtsogoleri+ wa cholowa chake.+
13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+