Genesis 31:55 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+ Genesis 48:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+ Genesis 50:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 50 Pamenepo Yosefe anakumbatira mtembo wa bambo ake+ ndipo analira kwambiri n’kuupsompsona.+ 2 Samueli 19:39 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 39 Tsopano anthu onse anayamba kuwoloka Yorodano, ndipo mfumu nayonso inawoloka. Koma mfumu inapsompsona+ Barizilai ndi kumudalitsa,+ kenako Barizilai anabwerera kwawo.
55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+
10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+
39 Tsopano anthu onse anayamba kuwoloka Yorodano, ndipo mfumu nayonso inawoloka. Koma mfumu inapsompsona+ Barizilai ndi kumudalitsa,+ kenako Barizilai anabwerera kwawo.