Genesis 31:55 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+ Rute 1:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Atatero iwo analiranso mokweza mawu. Kenako Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.+ 1 Samueli 20:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+ 1 Mafumu 19:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Zitatero, Elisa anasiya ng’ombe zamphongozo n’kuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikapsompsone kaye bambo anga ndi mayi anga,+ kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.” Machitidwe 20:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Pamenepo onse analira kwambiri, ndipo anakumbatira+ Paulo ndi kumupsompsona mwachikondi.+
55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+
14 Atatero iwo analiranso mokweza mawu. Kenako Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.+
41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+
20 Zitatero, Elisa anasiya ng’ombe zamphongozo n’kuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikapsompsone kaye bambo anga ndi mayi anga,+ kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.”