6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
24 Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo,+ Kuta, Ava,+ Hamati,+ ndi Sefaravaimu+ n’kuwakhazika m’mizinda ya Samariya,+ m’malo mwa ana a Isiraeli. Anthuwo anatenga Samariya n’kumakhala m’mizinda yake.