28 Nkhani zina zokhudza Yerobowamu ndi zonse zimene anachita, zochita zake zamphamvu ndiponso mmene anamenyera nkhondo, ndi mmene anabwezeretsera Damasiko+ ndi Hamati+ ku Yuda mu Isiraeli, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.