26 Ansembe ako aphwanya chilamulo changa modzionetsera,+ ndipo akuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa+ zinthu zoyera ndi zinthu wamba.+ Sanauze anthu kusiyana kwa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyera.+ Anyalanyaza sabata langa+ ndipo andichitira mwano pakati pawo.+