Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Ansembe ndi aneneri+ asochera chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Asokonezeka chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku+ chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Sakuonanso bwino ndipo zochita zawo zikusonyeza kuti sakuganiza bwino.

  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

  • Yeremiya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Pakuti aliyense wa iwo, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+

  • Yeremiya 8:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena, ndipo minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+ Pakuti kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu aliyense wa iwo akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+

  • Ezekieli 22:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Aneneri ako akukonza chiwembu mwa iwe.+ Iwo akukhadzula anthu+ ngati mkango wobangula umene wagwira nyama.+ Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali.+ Achulukitsa akazi amasiye mmenemo.+

  • Zefaniya 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Aneneri ake anali amwano ndi achinyengo.+ Ansembe ake anaipitsa zinthu zopatulika ndipo anaphwanya chilamulo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena