Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

  • Yeremiya 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+

  • Maliro 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.

      Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+

      Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.

  • Maliro 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+

      Amene anakhetsa magazi a anthu olungama a mumzindawo.+

  • Ezekieli 22:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Aneneri a mumzindawo apaka laimu machimo a atsogoleriwo.+ Aona masomphenya onama+ ndipo akuloserera atsogoleriwo zinthu zabodza.+ Iwo akunena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena