Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Ndipo anthu ophunzitsa chilamulo sanandidziwe.+ Abusa nawonso anaphwanya malamulo anga,+ ndipo aneneri anali kulosera m’dzina la Baala+ ndi kutsatira milungu yopanda phindu.+

  • Yeremiya 14:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndipo ndikapita kunja kwa mzinda, ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+ Komanso ndikalowa mkati mwa mzinda ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala.+ Aneneri ndi ansembe, onse ayenda njira zosiyanasiyana kupita kudziko limene sakulidziwa.’”+

  • Yeremiya 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova.

  • Mika 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Yehova wanena zimene zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+ Aneneri amenewo akutafuna chakudya ndi mano awo+ n’kumanena kuti, ‘Mtendere!’+ Koma munthu akapanda kuika chakudya m’kamwa mwawo, amakonzekera kumuthira nkhondo.+ Kwa iwo Mulungu wanena kuti,

  • Mika 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+

  • Zefaniya 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Aneneri ake anali amwano ndi achinyengo.+ Ansembe ake anaipitsa zinthu zopatulika ndipo anaphwanya chilamulo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena