14 Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+
39 Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+