11 Iwo anayamba kuimba molandizana potamanda+ ndi kuthokoza Yehova kuti, “iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kosatha kumene amakusonyeza kwa Isiraeli kudzakhala mpaka kalekale.”*+ Ndipo anthu onse anafuula mokweza kwambiri+ potamanda Yehova chifukwa cha kumangidwa kwa maziko a nyumba ya Yehova.