13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+
12 Tsopano Davide anali mwana wamwamuna wa Jese, Mwefurata+ wina wa ku Betelehemu, ku Yuda. Jese anali ndi ana aamuna 8+ ndipo m’masiku a Sauli iye anali atakalamba kale.