Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako ananyamuka kuchoka ku Beteliko. Padakali mtunda wautali ndithu kuti afike ku Efurata,+ inafika nthawi yoti Rakele abereke, koma poberekapo anali kuvutika kwambiri.+

  • Genesis 35:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Umu ndi mmene Rakele anamwalirira, ndipo anamuika m’manda ali m’njira popita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+

  • Rute 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Munthuyo dzina lake anali Elimeleki, ndipo mkazi wake anali Naomi. Mayina a ana akewo anali Maloni ndi Kiliyoni. Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata+ wa ku Yuda. Ndipo anafika m’dziko la Mowabu ndi kukhazikika kumeneko.

  • Rute 4:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Obedi anabereka Jese,+ ndipo Jese anabereka Davide.+

  • 1 Samueli 16:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli+ mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta m’nyanga yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”+

  • 1 Samueli 17:58
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 58 Ndiyeno Sauli anamufunsa kuti: “Mnyamata iwe, bambo wako ndani?” Poyankha Davide anati: “Ndine mwana wa mtumiki wanu Jese,+ wa ku Betelehemu.”+

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Mateyu 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 ‘Iwe Betelehemu+ wa m’dziko la Yuda, suli mzinda waung’ono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira+ amene adzaweta+ anthu anga, Aisiraeli.’”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena