Levitiko 26:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ine ndidzakukanani,* ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+ Numeri 27:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse,+ kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda m’busa.”+ Deuteronomo 28:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+ Zekariya 10:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Aterafi*+ amalankhula zoipa. Ochita zamaula amaona masomphenya onama+ ndipo amafotokoza maloto opanda pake. Iwo saphula kanthu polimbikitsa anthu.+ N’chifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.+ Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda m’busa.+
17 Ine ndidzakukanani,* ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+
17 Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse,+ kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda m’busa.”+
25 Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+
2 Aterafi*+ amalankhula zoipa. Ochita zamaula amaona masomphenya onama+ ndipo amafotokoza maloto opanda pake. Iwo saphula kanthu polimbikitsa anthu.+ N’chifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.+ Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda m’busa.+