30 Koma musadye nyama ya nsembe yamachimo imene ena mwa magazi+ ake adzalowa nawo m’chihema chokumanako kuti aphimbire machimo m’malo oyerawo. Imeneyo muziitentha ndi moto.
10 Pakuti ngati pamene tinali adani,+ tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake,+ nanji tsopano pamene tayanjanitsidwa, tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake.+
17 Chotero, iye anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.+ Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo+ kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu.+