Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo ndani angakhale ndi mphamvu zomangira Mulunguyo nyumba?+ Pakuti kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, ndi kosakwanira kuti akhaleko.+ Ndiye ine ndine ndani+ kuti ndimumangire nyumba, kupatulapo yofukiziramo nsembe yautsi pamaso pake?+

  • Nehemiya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Inu ndinu Yehova, inu nokha.+ Ndinu amene munapanga kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba ndi makamu ake onse.+ Ndinu amene munapanga dziko lapansi+ ndi zonse zili momwemo+ komanso nyanja+ ndi zonse zili momwemo.+ Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu+ akumwamba amakugwadirani.

  • Salimo 148:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+

      Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+

      Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+

  • Yesaya 40:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo?

  • Machitidwe 17:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena