9 Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati.
20 Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Pomalizira pake iye anapita popanda womumvera chisoni.+ Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide,+ koma osati m’manda a mafumu.+