Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400 ndipo Sezibazara+ anabweretsa zonsezi ku Yerusalemu. Anatenganso anthu amene anagwidwa ukapolo+ kuchoka nawo ku Babulo n’kupita nawo ku Yerusalemu.

  • Ezara 5:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Komanso, ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara anazitenga m’kachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, n’kupita nazo kukachisi wa ku Babulo,+ mfumu Koresi+ inazichotsa m’kachisi wa ku Babuloyo. Ndiyeno zinaperekedwa kwa Sezibazara,+ munthu amene Koresi anamuika kukhala bwanamkubwa.+

  • Danieli 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+

  • Danieli 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo+ anaitanitsa ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga m’kachisi ku Yerusalemu. Anaitanitsa zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena apambali amweremo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena