1M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo,+ m’mwezi wa 6, pa tsiku loyamba la mweziwo, mawu a Yehova anafika kwa Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ bwanamkubwa wa Yuda,+ ndi kwa Yoswa+ mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe. Mawuwa anafika kwa anthu amenewa kudzera mwa mneneri Hagai+ kuti:
14 Yehova analimbikitsa+ Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda, Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe ndi anthu ena onse. Choncho iwo anapita kukagwira ntchito panyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wawo.+