-
Ezara 4:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 n’cholinga choti mufufuze m’buku la mbiri+ ya makolo anu. Mukafufuza m’bukulo mupeza kuti mzinda umenewu ndi mzinda woukira ndi wowonongetsa chuma cha mafumu ndi zigawo za mayiko. Mupezanso kuti mumzinda umenewu mwakhala muli anthu oyambitsa kupanduka kuyambira kalekale. N’chifukwa chake mzindawu uli bwinja.+
-