Yobu 35:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Iwo amangokhalira kulirira thandizo, koma iye sawayankha+Chifukwa cha kunyada+ kwa anthu oipa. Salimo 18:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+ Miyambo 28:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo,+ ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+ Yeremiya 11:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndiwagwetsera tsoka+ limene sadzatha kulithawa.+ Iwo adzandiitana kuti ndiwathandize, koma sindidzawamvera.+ Yakobo 4:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa,+ kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.+
41 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+
9 Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo,+ ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+
11 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndiwagwetsera tsoka+ limene sadzatha kulithawa.+ Iwo adzandiitana kuti ndiwathandize, koma sindidzawamvera.+
3 Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa,+ kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.+