15 Mukatambasula manja anu,+ ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+ ine sindimvetsera.+ Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.+
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+