Yobu 23:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+ Salimo 37:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa,+Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+ Yeremiya 12:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Inu Yehova, mumandidziwa bwino.+ Mumandiona ndipo mumasanthula mtima wanga kuti muone ngati uli wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,+ ndipo aikeni padera kuyembekezera tsiku lokaphedwa. 2 Timoteyo 2:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire,+ ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova+ aleke kuchita zosalungama.”+ 1 Petulo 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+
10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+
3 Inu Yehova, mumandidziwa bwino.+ Mumandiona ndipo mumasanthula mtima wanga kuti muone ngati uli wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,+ ndipo aikeni padera kuyembekezera tsiku lokaphedwa.
19 Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire,+ ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova+ aleke kuchita zosalungama.”+
12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+