2 Mafumu 20:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+ 1 Mbiri 29:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu. Salimo 17:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+ Salimo 44:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+ Yeremiya 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma Yehova wa makamu amaweruza mwachilungamo.+ Amafufuza impso ndi mtima.+ Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango, pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+
3 “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+
17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu.
3 Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+
20 Koma Yehova wa makamu amaweruza mwachilungamo.+ Amafufuza impso ndi mtima.+ Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango, pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+