Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 22:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Yehova utamva zimene ndanena zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chodabwitsa ndi temberero,+ unang’amba+ zovala zako n’kuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva,” ndiwo mawu a Yehova.+

  • Salimo 34:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+

      Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.+

  • Yesaya 57:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pakuti Wapamwamba ndi Wokwezeka,+ yemwe adzakhalepo kwamuyaya+ ndiponso yemwe dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti: “Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyera.+ Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa,+ kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+

  • Luka 18:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena